Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 24:40-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pace, adzatumiza mthenga wace pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamteogere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi ku nyumba ya atate wanga;

41. ukatero udzakhala wosacimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abate anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosacimwa pa malumbiro ako.

42. Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m'mene ndinkamo ine;

43. taonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene aturuka kudzatunga madzi, ndikati kwa iye, Ndipatse madzi ndimwe pang'ono m'mtsuko mwako;

44. ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamila zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga.

Werengani mutu wathunthu Genesis 24