Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 24:27-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamuamene sanasiya mbuyanga wopanda cifundo cace ndi zoona zace: koma ine Yehova Wanditsogolera m'njira ya ku nyumba ya abale ace a mbuyanga.

28. Namwaliyo ndipo anathamanga nawauza zimenezo ku nyumba ya amace.

29. Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wace dzina lace Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.

30. Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wace, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wace, akuti, Cotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamila pakasupe.

31. Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? cifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamila.

32. Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamila, napatsa ngamila maudzu ndi cakudya, ndi madzi akusamba mapazi ace ndi mapazi a iwo amene anali naye.

33. Ndipo anaika cakudya pamaso pace: koma anati, Sindidzadya ndisananene cimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.

34. Ndipo anati, Ine ndine mnyamata wa Abrahamu.

35. Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo anakula kwakukuru; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golidi, ndi akapolo ndi adzakazi, oeli ngamila ndi aburu.

36. Ndipo Sara mkazi wace wa mbuyanga anambalira mbuyanga mwana wamwamuna, mkaziyo anali wokalamba; ndipo anampatsa mwanayo zonse ali nazo.

37. Ndipo mbuyanga anandilumbiritsa ine kuti, Usamteogere mwana wanga mkazi wa ana akazi a Kanani, m'dziko mwao m'mene ndikhala ine;

38. koma udzanke ku nyumba ya atate wanga, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga mkazi.

39. Ndipo ndinati kwa mbuyanga, Kapena mkazi sadzanelitsata ine.

40. Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pace, adzatumiza mthenga wace pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamteogere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi ku nyumba ya atate wanga;

41. ukatero udzakhala wosacimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abate anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosacimwa pa malumbiro ako.

42. Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m'mene ndinkamo ine;

43. taonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene aturuka kudzatunga madzi, ndikati kwa iye, Ndipatse madzi ndimwe pang'ono m'mtsuko mwako;

Werengani mutu wathunthu Genesis 24