Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 24:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamuamene sanasiya mbuyanga wopanda cifundo cace ndi zoona zace: koma ine Yehova Wanditsogolera m'njira ya ku nyumba ya abale ace a mbuyanga.

28. Namwaliyo ndipo anathamanga nawauza zimenezo ku nyumba ya amace.

29. Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wace dzina lace Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.

30. Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wace, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wace, akuti, Cotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamila pakasupe.

31. Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? cifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamila.

32. Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamila, napatsa ngamila maudzu ndi cakudya, ndi madzi akusamba mapazi ace ndi mapazi a iwo amene anali naye.

33. Ndipo anaika cakudya pamaso pace: koma anati, Sindidzadya ndisananene cimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.

Werengani mutu wathunthu Genesis 24