Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 21:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anayang'anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamcitira iye monga ananena.

2. Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu m'ukalamba wace mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye.

3. Ndipo Abrahamu anamucha dzina lace la mwana wace wamwamuna amene anabala iye, amene anambalira iye Sara, Isake.

4. Ndipo Abrahamu anamdula mwana wace wamwamuna Isake pamene anali wa masiku ace asanu ndi atatu, monga Mulungu anamlamulira iye.

5. Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isake mwana wace.

6. Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine.

7. Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna m'ukalamba wace.

8. Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero akuru tsiku lomwe analetsedwa Isake kuyamwa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 21