Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 2:19-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazicha; ndipo maina omwe onse anazicha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.

20. Adamu ndipo anazicha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m'mlengalenga ndi zamoyo zonse za m'thengo: koma kwa Adamu sanapezedwa womthangatira iye.

21. Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikuru, ndipo anagona: ndipo anatengako nthiti yace imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pace:

22. ndipo nthitiyo anaicotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu.

23. Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye pfupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzachedwa Mkazi, cifukwa anamtenga mwa mwamuna.

24. Cifukwa cotero mwamuna adzasiya atate wace ndi amace nadzadziphatika kwa mkazi wace: ndipo adzakhala thupi limodzi.

25. Onse awiri ndipo anali amarisece, mwamuna ndi mkazi wace, ndipo analibe manyazi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 2