15. Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Eriene kuti aulime nauyang'anire.
16. Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m'munda udyeko;
17. koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa, usadye umenewo; cifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.
18. Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthuakhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.
19. Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazicha; ndipo maina omwe onse anazicha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.
20. Adamu ndipo anazicha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m'mlengalenga ndi zamoyo zonse za m'thengo: koma kwa Adamu sanapezedwa womthangatira iye.
21. Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikuru, ndipo anagona: ndipo anatengako nthiti yace imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pace:
22. ndipo nthitiyo anaicotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu.
23. Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye pfupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzachedwa Mkazi, cifukwa anamtenga mwa mwamuna.
24. Cifukwa cotero mwamuna adzasiya atate wace ndi amace nadzadziphatika kwa mkazi wace: ndipo adzakhala thupi limodzi.
25. Onse awiri ndipo anali amarisece, mwamuna ndi mkazi wace, ndipo analibe manyazi.