Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 18:30-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzacita.

31. Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca makumi awiri.

32. Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwakhumim'menemo: Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca khumi.

33. Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 18