Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 18:25-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzacita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?

26. Ndipo anati Yehova, Ndikapeza m'Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi, ndidzasiya malo onse cifukwa ca iwo.

27. Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine pfumbi ndi phulusa:

28. kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mudzi wonse cifukwa ca kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.

29. Ndipo ananenanso kwa iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca makumi anai.

30. Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzacita.

31. Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca makumi awiri.

32. Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwakhumim'menemo: Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca khumi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 18