Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 18:22-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo anthuwo anatembenuka nacoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova.

23. Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa?

24. Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi; kodi mudzaononga, simudzasiya malowa cifukwa ca olungama makumi asanu ali momwemo?

25. Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzacita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?

26. Ndipo anati Yehova, Ndikapeza m'Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi, ndidzasiya malo onse cifukwa ca iwo.

27. Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine pfumbi ndi phulusa:

28. kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mudzi wonse cifukwa ca kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.

29. Ndipo ananenanso kwa iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca makumi anai.

Werengani mutu wathunthu Genesis 18