Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 18:13-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba?

14. Kodi ciripo cinthu comlaka Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yace, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.

15. Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; cifukwa anaopa, Ndipo anati, lai; koma unaseka.

16. Ndipo anthuwo anauka kucokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza.

17. Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu cimene ndicita?

18. Pakuti Abrahamu adzakhala ndithu wamkuru ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsika mwa iye?

19. Cifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ace ndi banja lace la pambuyo pace, kuti asunge njira ya Yehova, kucita cilungamo ndi ciweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu comwe anamnenera iye.

20. Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukuru, ndipo popeza kucimwa kwao kuli kulemera ndithu,

21. ndidzatsikatu ndikaone ngati anacita monse monga kulira kwace kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa.

22. Ndipo anthuwo anatembenuka nacoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova.

23. Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa?

24. Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi; kodi mudzaononga, simudzasiya malowa cifukwa ca olungama makumi asanu ali momwemo?

25. Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzacita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?

Werengani mutu wathunthu Genesis 18