Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 16:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo anacha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang'ana pambuyo pace pa iye amene wakundiona ine?

14. Cifukwa cace citsimeco cinachedwa Beerelahai-roi; taonani ciri pakati pa Kadese ndi Berede.

15. Ndipo Hagara anambalira Abramumwana wamwamuna, ndipo Abramu anacha dzina la mwana wace amene anambalira iye Hagara, lsmayeli.

16. Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi cimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismayeli.

Werengani mutu wathunthu Genesis 16