Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 14:21-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge cuma iwe wekha.

22. Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkurukuru, mwini kumwamba ndi dziko lapansi,

23. kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale cingwe ca nsapato, ngakhale kanthu kali konse kako, kuti unganene, Ndamlemeza Abramu;

24. koma cokhaci anadya anyamata, ndi gawo lao la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Aneri, Esikolo, ndi Mamre, iwo atenge gawo lao.

Werengani mutu wathunthu Genesis 14