Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 13:16-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga pfumbi lapansi: cotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga pfumbi lapansi, comweconso mbeu yako idzawerengedwa.

17. Tauka, nuyendeyendc m'dzikoli m'litari mwace ndi m'mimba mwace; cifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo.

18. Ndipo Abramu anasuntha hema wace nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre, imene iri m'Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.

Werengani mutu wathunthu Genesis 13