Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 11:4-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo anati, Tiyeni, timange mudzi ndi nsanja, pamutu pace pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike pa dziko lonse lapansi.

5. Ndipo Yehova anatsikira kudzaona mudzi ndi nsanja imene analinkumanga ana a anthu.

6. Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali naco cinenedwe cao cimodzi; ndipo ici ayamba kucita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kucita.

7. Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze cinenedwe cao, kuti wina asamvere cinenedwe ca mnzace.

8. Ndipo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mudzi.

9. Cifukwa cace anacha dzina lace Babele; pakuti kumeneko Yehova anasokoneza cinenedwe ca dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi.

10. Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakasadi, citapita cigumula zaka ziwiri;

11. ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakasadi, nabala ana amuna ndi akazi.

12. Ndipo Aripakasadi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zisanu, nabala Sela;

13. ndipo Aripakasadi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Sela, nabala ana amuna ndi akazi.

14. Ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Ebere;

15. ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Ebere, nabala ana amuna ndi akazi.

16. Ndipo Ebere anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zinai, nabala Pelege;

17. ndipo Ebere anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza makumi awiri, atabala Pelege, nabala ana amuna ndi akazi.

18. Ndipo Pelege anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala, Reu;

Werengani mutu wathunthu Genesis 11