Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 11:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo dziko lapansi linali la cinenedwe cimodzi ndi cilankhulidwe cimodzi.

2. Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum'mawa, anapeza cigwa m'dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko.

3. Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziocetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.

4. Ndipo anati, Tiyeni, timange mudzi ndi nsanja, pamutu pace pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike pa dziko lonse lapansi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 11