Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 10:5-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Amenewo ndipo anagawa zisi za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa cinenedwe cao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.

6. Ndi ana amuna a Hamu: Kusi, ndi Mizraimu, ndi Puti, ndi Kanani.

7. Ndi ana amuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedane.

8. Ndipo Kusi anabala Nimrode; ndipo iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko lapansi.

9. Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova: cifukwa cace kunanenedwa, Monga Nimrode mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.

10. Ndipo kuyamba kwace kwa ufumu wace kunali Babele, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.

11. M'dziko momwemo iye anaturuka kunka ku Ashuri, namanga Nineve, ndi mudzi wa Rehoboti, ndi Kala,

12. ndi Resene pakati pa Nineve ndi Kala: umenewo ndi mudzi waukuru.

13. Mizraimu ndipo anabala Ludimu, ndi Anamimu, ndi Lehabimu, ndi Nafituhimu,

14. ndi Patrusimu, ndi Kasiluhimu, m'menemo ndipo anaturuka Afilisti, ndi Kafitorimu.

15. Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wace, ndi Heti:

16. ndi Ajebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi;

17. ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini;

18. ndi Aaravadi, ndi Aazemari, ndi Ahamati; pambuyo pace pamenepo ndipo mabanja a Akanani anafalikira.

19. Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.

20. Amenewa ndi ana amuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.

Werengani mutu wathunthu Genesis 10