Ndipo taonani, munthu wobvala bafutayo, wokhala ndi zolembera nazo m'cuuno mwace, anabweza mau, ndi kuti, Ndacita monga munandilamulira ine.