Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 8:3-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo anatambasula conga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati pa dziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku citseko ca cipata ca bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje locititsa nsanje.

4. Ndipo taonani, pomwepo panali ulemerero wa Mulungu wa lsrayeli, monga mwa maonekedwe ndinawaona ku cidikha cija.

5. Pamenepo ananena ndi ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza maso ako ku njira yoloza kumpoto. Ndipo ndinakweza maso anga ku njira yoloza kumpoto, ndipo taonani, kumpoto kwa cipata ca guwa la nsembe fano ili la nsanje polowera pace.

6. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzicita? zonyansa zazikulu nyumba ya Israyeli irikuzicita kuno, kuti ndicoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.

7. Ndipo anadza nane ku cipata ca kubwalo, ndipo popenya ine, taonani, pobooka palinga.

8. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, booletsa kulinga; ndipo nditabooletsa palinga, ndinaona khomo.

9. Ndipo anati kwa ine, Lowa, kapenye zonyansa zoipa alikuzicita komweko.

10. M'mwemo ndinalowa ndi kupenya, ndipo taonani, maonekedwe ali onse a zokwawa, ndi zirombo zonyansa, ndi mafano onse a nyumba ya Israyeli, zolembedwa pakhoma pozungulira ponse.

11. Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israyeli, ndi pakati pao panaima Jazaniya mwana wa Safana munthu ali yense ndi mbale yace ya zofukiza m'dzanja lace; ndi pfungo lace la mtambo wa zonunkhira linakwera.

12. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi cocita akulu a nyumba ya lsrayeli mumdima, ali yense m'cipinda cace ca zifanizo? pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 8