Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 7:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

2. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova kwa dziko la Israyeli, Kwatha; kwafika kutha kwace pa ngondya zinai za dziko.

3. Tsopano kwakudzera kutha kwako, ndipo ndidzakutumizira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zanse.

4. Ndipo diso langa silidzakulekerera, sindidzacita cifundo, koma ndidzakubwezera njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

5. Atero Yehova Mulungu, Coipa, coipa ca pa cokha, taona cirinkudza.

6. Kutha kwafika, kwafika kutha, kwakugalamukira, taona kwafika.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 7