Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 48:24-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndi ku malire a Benjamini, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Simeoni, gawo limodzi.

25. Ndi ku malire a Simeoni kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Isakara, limodzi.

26. Ndi ku malire a Isakara, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Zebuloni, limodzi.

27. Ndi ku malire a Zebuloni, kuyambira ku mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Gadi, limodzi.

28. Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwela, kuloza kumwela, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati ndi Kadesi, ku mtsinje wa Aigupto, kufikira ku nyanja yaikuru.

29. Ili ndi dziko muligawire mafuko a Israyeli ndi kucita maere, likhale colowa cao; ndipo awa ndi magawo ao, ati Ambuye Yehova.

30. Ndipo malekezero a mudzi ndi awa: mbali ya kumpoto avese mabango zikwi zinai mphambu mazana asanu;

31. ndi zipata za mudzi zidzakhala monga mwa maina a mafuko a Israyeli; zipata zitatu kumpoto: cipata cimodzi ca Rubeni, cipata cimodzi ca Yuda, cipata cimodzi ca Levi;

32. ndi ku mbali ya kum'mawa zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: cipata cimodzi ca Yosefe, cipata cimodzi ca Benjamini, cipata cimodzi ca Dani;

33. ndi ku mbali ya kumwela ayese zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: cipata cimodzi ca Simeoni, cipata cimodzi ca Isakara, cipata cimodzi ca Zebuloni;

34. ku mbali ya kumadzulo zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zace zitaru; cipata cimodzi ca Gadi, cipata cimodzi ca Aseri, cipata cimodzi ca Nafitali.

35. Pozungulira pace ndipo mabango zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mudziwo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 48