Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 48:22-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Kuyambira tsono dziko la Alevi kufikira dziko la mudzi, ndiwo a pakati pa magawo ace a kalonga, pakati pa malire a Yuda ndi malire a Benjamini, kukhale kwa kalonga.

23. Kunena za mafuko otsala tsono, kuyambira ku mbali ya kum'mawa kufikita mbali ya kumadzulo, Benjamini akhale nalo gawo limodzi.

24. Ndi ku malire a Benjamini, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Simeoni, gawo limodzi.

25. Ndi ku malire a Simeoni kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Isakara, limodzi.

26. Ndi ku malire a Isakara, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Zebuloni, limodzi.

27. Ndi ku malire a Zebuloni, kuyambira ku mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Gadi, limodzi.

28. Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwela, kuloza kumwela, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati ndi Kadesi, ku mtsinje wa Aigupto, kufikira ku nyanja yaikuru.

29. Ili ndi dziko muligawire mafuko a Israyeli ndi kucita maere, likhale colowa cao; ndipo awa ndi magawo ao, ati Ambuye Yehova.

30. Ndipo malekezero a mudzi ndi awa: mbali ya kumpoto avese mabango zikwi zinai mphambu mazana asanu;

31. ndi zipata za mudzi zidzakhala monga mwa maina a mafuko a Israyeli; zipata zitatu kumpoto: cipata cimodzi ca Rubeni, cipata cimodzi ca Yuda, cipata cimodzi ca Levi;

32. ndi ku mbali ya kum'mawa zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: cipata cimodzi ca Yosefe, cipata cimodzi ca Benjamini, cipata cimodzi ca Dani;

33. ndi ku mbali ya kumwela ayese zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: cipata cimodzi ca Simeoni, cipata cimodzi ca Isakara, cipata cimodzi ca Zebuloni;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 48