Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 48:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Maina a mafuko tsono ndi awa: Kuyambira nsonga ya kumpoto, ku mbali ya njira ya ku Heteloni, polowera ku Hamati, Hazarenani ku malire a Damasiko kumpoto, ku mbali ya ku Hamati; ndi mbali zace zilinge kum'mawa ndi kumadzulo; Dani akhale nalo gawo limodzi.

2. Ndi m'malire a Dani, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Aseri, limodzi.

3. Ndi m'malire a Aseri, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Nafitali, limodzi.

4. Ndi m'malire a Nafitali, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Manase, limodzi.

5. Ndi m'malire a Manase, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Efraimu, limodzi.

6. Ndi m'malire a Efraimu, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Rubeni, limodzi.

7. Ndi m'malire a Rubeni, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Yuda, limodzi.

8. Ndi m'malire a Yuda, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, pakhale copereka a mucipereke, mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwace, ndi m'litali mwace lilingane ndi magawo enawo, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; ndi malo opatulika akhale pakati pace.

9. Copereka mucipereke kwa Yehova cikhale ca mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace.

10. Ndipo m'mwemo mudzakhala copereka copatulika ca ansembe kumpoto, zikwi makumi awiri mphambu zisanu a m'litali mwace, ndi kumadzulo zikwi khumi kupingasa kwace, ndi kum'mawa zikwi khumi kupingasa kwace, ndi kumwela zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace; ndi pakati pace pakhale malo opatulika a Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 48