Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 39:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, nenera motsutsana naye Gogi, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Gogi, iwe mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;

2. ndipo ndidzakutembenuza, ndi kukutsogolera, ndi kukweza iwe ucoke ku malekezero a kumpoto; ndipo ndidzadza nawe ku mapiri a Israyeli;

3. ndipo ndidzakantha uta wako kuucotsa m'dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mibvi yako ku dzanja lako lamanja.

4. Udzagwa pa mapiri a Israyeli, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zirombo za kuthengo, akuyese cakudya.

5. Udzagwa kuthengo koyera, pakuti ndanena ndine, ati Ambuye Yehova.

6. Ndipo ndidzatumizira moto Magogi, ndi iwo okhala mosatekeseka m'zisumbu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

7. Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israyeli, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 39