Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 38:9-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo udzakwera udzadza ngati mkuntho, udzanga mtambo kuphimba dziko, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe.

10. Atero Ambuye Yehova, Kudzacitika tsiku ilo kuti m'mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira ciwembu coipa,

11. nudzati, Ndidzakwera kumka ku dziko la midzi yopanda malinga, ndidzamka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mipingiridzo, kapena zitseko;

12. kulanda ndi kufunkha zao, kubweza dzanja lako liononge mopasuka muli anthu tsopano, liononge mtundu wa anthu osonkhanidwa mwa amitundu, odzionera zoweta ndi cuma, okhala pakati pa dziko.

13. Seba, ndi Dedani, ndi amalonda a Tarisi, ndi misona yace yonse ya mikango adzati kwa iwe, Wadza kodi kudzafunkha? wasonkhanitsa kodi msonkhano wako kulanda, kucoka nazo siliva ndi golidi, kucoka nazo zoweta ndi cuma, kulanda zankhondo zambiri?

14. Cifukwa cace nenera, wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa Gogi, Atero Ambuye Yehova, Tsiku ilo, pokhala mosatekeseka anthu anga Israyeli, sudzacidziwa kodi?

15. Ndipo udzaturuka m'malo mwako m'malekezero a kumpoto, iwe ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe, onsewo apakavalo, msonkhano waukuru ndi nkhondo yaikuru;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 38