Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 38:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kwa Gogi, wa ku dziko la Magogi, ndiye mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;

3. nunenere motsutsana naye, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe, Gogi iwe, mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;

4. ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m'cibwano mwako ndi zokowera, ndi kukuturutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo obvala mokwanira onsewo, msonkhano waukuru ndi zikopa zocinjiriza, onsewo ogwira, bwino malupanga;

5. Perisiya, Kusi, ndi Puti pamodzi nao, onsewo ndi cikopa ndi cisoti cacitsulo;

6. Gomeri ndi magulu ace onse, nyumba ya Togarima, ku malekezero a kumpoto, ndi magulu ace onse, mitundu yambiri pamodzi ndi iwe.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 38