Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 38:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kwa Gogi, wa ku dziko la Magogi, ndiye mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;

3. nunenere motsutsana naye, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe, Gogi iwe, mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;

4. ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m'cibwano mwako ndi zokowera, ndi kukuturutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo obvala mokwanira onsewo, msonkhano waukuru ndi zikopa zocinjiriza, onsewo ogwira, bwino malupanga;

5. Perisiya, Kusi, ndi Puti pamodzi nao, onsewo ndi cikopa ndi cisoti cacitsulo;

6. Gomeri ndi magulu ace onse, nyumba ya Togarima, ku malekezero a kumpoto, ndi magulu ace onse, mitundu yambiri pamodzi ndi iwe.

7. Ukonzekeretu, Inde udzikonzeretu, iwe ndi msonkhano wako wonse unakusonkhanira, nukhale iwe mtsogoleri wao.

8. Atapita masiku ambiri udzakumbukirika; zaka zotsiriza udzalowa m'dziko lobwezedwa lopulumuka lupanga, losonkhanidwa lituruke m'mitundu yambiri ya anthu, pa mapiri a Israyeli, amene adakhala acipululu cikhalire; koma liturutsidwa m'mitundu ya anthu, ndipo adzakhala mosatekeseka onsewo.

9. Ndipo udzakwera udzadza ngati mkuntho, udzanga mtambo kuphimba dziko, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe.

10. Atero Ambuye Yehova, Kudzacitika tsiku ilo kuti m'mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira ciwembu coipa,

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 38