Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 36:28-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo mudzakhala m'dziko ndinapatsa makolo anulo, ndipo mudzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu.

29. Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumcurukitsa, osaikiranso inu njala.

30. Ndipo ndidzacurukitsa zobala za mitengo, ndi zipatso za m'munda, kuti musalandirenso citonzo ca njala mwa amitundu.

31. Pamenepo mudzakumbukila njira zanu zoipa, ndi zocita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, cifukwa ca mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.

32. Dziwani kuti sindicita ici cifukwa ca inu, ati Ambuye Yehova; citani manyazi, dodomani, cifukwa ca njira zanu, nyumba ya Israyeli inu.

33. Atero Ambuye Yehova, Tsiku loti ndikuyeretsani kukucotserani mphulupulu zanu zonse, ndidzakhalitsa anthu m'midzimo; ndi pamabwinja padzamangidwa.

34. Ndi dziko lacipululu lidzalimidwa, cinkana linali lacipululu pamaso pa onse opitako.

35. Ndipo adzati, Dziko ili lacipululu lasanduka ngati munda wa Edene, ndi midzi yamabwinja, ndi yacipululu, ndi yopasuka, yamangidwa malinga, muli anthu m'mwemo.

36. Pamenepo amitundu otsala pozungulira panu adzadziwa kuti Ine Yehova ndamanga malo opasuka, ndi kubzala pamene panali cipululu; Ine Yehova ndanena ndidzacita.

37. Atero Ambuye Yehova, Ici comwe adzandipempha a nyumba ya Israyeli ndiwacitire ici, ndidzawacurukitsira anthu ngati nkhosa.

38. Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa madyerero ace oikika, momwemo midzi yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 36