1. Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2. Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako ku phiri la Seiri, nulinenere molitsutsa;
3. nuti nalo, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndiipidwa nawe phiri la Seiri, ndipo ndidzakutambasulira dzanja langa, ndi kukusanduliza lacipululu ndi lodabwitsa.
4. Ndidzapasula midzi yako, nudzakhala lacipululu; ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
5. Popeza uli nao udani wosatha, waperekanso ana a Israyeli ku mphamvu ya lupanga m'nthawi ya tsoka lao, mu nthawi ya mphulupulu yotsiriza;
6. cifukwa cace, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndikukonzeratu uphedwe, ndi mwazi udzakulondola; popeza sunadana nao mwazi, mwazi udzakulondola.