Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 31:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, mwezi wacitatu, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, nena kwa Farao mfumu ya Aigupto ndi aunyinji ace, Ufanana ndi yani m'ukulu wako?

3. Taona, Asuri anali mkungudza wa ku Lebano ndi nthambi zokoma zobvalira, wautali msinkhu, kunsonga kwace ndi kumitambo.

4. Madzi anaumeretsa, cigumula cinaukulitsa, mitsinje yace inayenda, nizungulira munda wace, nipititsa micera yace ku mitengo yonse ya kuthengoko.

5. Cifukwa cace msinkhu wace unaposa mitengo yonse ya kuthengo, ndi nthambi zace zinacuruka, ndi nthawi zace zinatalika, Cifukwa ca madzi ambiri pophuka uwu.

6. Mbalame zonse za m'mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zace, ndi pansi pa nthawi zace zinaswana nyama zonse za kuthengo, ndi pa mthunzi wace inakhala mitundu yonse yaikuru ya anthu.

7. M'mwemo unakoma m'ukulu wace, m'kutalika kwa nthawi zace, popeza muzu wace unakhala ku madzi ambiri.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 31