Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 30:7-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo adzakhala opasuka pakati pa maiko opasuka, ndi midzi yace idzakhala pakati pa midzi yopasuka.

8. Ndipo adzadziwa, kuti Ine ndine Yehova, nditaika moto m'Aigupto, naonongeka onse akumthandiza.

9. Tsiku ilo mithenga idzaturuka pamaso panga m'zombo kuopsa Akusi osalabadira; ndipo kudzakhala kuwawa kwakukuru pakati pao, monga tsiku la Aigupto, pakuti taona, likudza.

10. Atero Ambuye Yehova, Ndidzaleketsa kusokosera kwa Aigupto ndi dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo.

11. Iye ndi anthu ace pamodzi naye, woopsa amitundu, adzatengedwa aliononge dzikolo, nadzasololera Aigupto malupanga ao, ndi kudzaza dziko ndi ophedwa.

12. Ndipo ndidzaphwetsa mitsinje, ndi kugulira dziko m'dzanja la anthu oipa, ndipo ndidzalisandutsa likhale dziko lopasuka, ndi zonse ziri m'mwemo mwa dzanja la alendo; Ine Yehova ndacinena.

13. Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pace ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wocokera ku Aigupto, ndipo ndidzaopsa dziko la Aigupto.

14. Ndipo ndidzasandutsa Patro labwinja, ndi kuika moto m'Zoani, ndi kukwaniritsa maweruzo m'No.

15. Ndipo ndidzatsanulira ukali wanga pa Sini, polimbika peni peni pa Aigupto, ndi kulikha aunyinji a No.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 30