Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 30:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pakuti layandikira tsiku, layandikira tsiku la Yehova, tsiku lamitambo, ndiyo nyengo ya amitundu.

4. Ndi lupanga lidzadzera Aigupto, ndi m'Kusi mudzakhala kuwawa kwakukuru, pakugwa ophedwa m'Aigupto; ndipo adzacotsa aunyinji ace, ndi maziko ace adzagadamuka,

5. Kusi, ndi Puti, ndi Ludi, ndi osokonezeka onse, ndi Kubi, ndi anthu a dziko lopangana nao, adzagwa pamodzi nao ndi lupanga.

6. Atero Yehova, Iwonso ocirikiza Aigupto adzagwa, ndi mphamvu yace yodzikuza idzatsika, kuyambira nsanja ya Sevene adzagwa m'kati mwace ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.

7. Ndipo adzakhala opasuka pakati pa maiko opasuka, ndi midzi yace idzakhala pakati pa midzi yopasuka.

8. Ndipo adzadziwa, kuti Ine ndine Yehova, nditaika moto m'Aigupto, naonongeka onse akumthandiza.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 30