Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 29:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Muja anakugwira ndi dzanja unatyoka, ndi kulasa mapewa ao onse; ndi muja anakutsamira unatyoka, ndi kuwagwedeza ziuno zao zonse.

8. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, ndikudzera ndi lupanga, ndi kukulikhira munthu ndi nyama.

9. Ndi dziko la Aigupto lidzakhala lopasuka ndi labwinja; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anati, Mtsinjewo ndi wanga, ndinaulenga ndine.

10. Cifukwa cace taona, nditsutsana ndi iwe ndi mitsinje yako, ndipo ndidzasandutsa dziko la Aigupto likhale lopasuka konse, ndi labwinja, kuyambira nsanja ya Sevene kufikira malire a Kusi.

11. Silidzapitamo phazi la munthu, kapena phazi la nyama losapitamo, losakhalamo anthu zaka makumi anai.

12. Ndipo ndidzasandutsa dziko la Aigupto labwinja pakati pa maiko a mabwinja; ndi midzi yace pakati pa midzi yopasuka idzakhala yabwinja zaka makumi anai; ndipo ndidzamwaza Aaigupto mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.

13. Pakuti atero Ambuye Yehova, Zitatha zaka makumi anai ndidzasonkhanitsa Aaigupto ku mitundu ya anthu kumene anamwazikirako;

14. ndipo ndidzabweza undende wa Aigupto, ndi kuwabwezera ku dziko la Patro, ku dziko la kubadwa kwao, ndi komweko adzakhala ufumu wopepuka,

15. Udzakhala wopepuka wa maufumu onse, sudzadzikwezanso pa amitundu; ndipo ndidzawacepsa, kuti asacitenso ufumu pa amitundu.

16. Ndipo sudzakhalanso cotama ca nyumba ya Israyeli, kukumbutsa mphulupulu, pakuwatembenukira kuwatsata; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 29