Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 27:26-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Opalasa ako anakufikitsa ku madzi akuru; mphepo ya kum'mawa inakutyola m'kati mwa nyanja,

27. Cuma cako, zako zogulana nazo malonda ako, amarinyero ako, ndi oongolera ako, amisiri ako, ndi ogulitsa malonda ako, ndi ankhondo ako onse okhala mwa iwe, pamodzi ndi msonkhano wonse uli pakati pa iwe, adzagwa m'kati mwa nyanja tsiku la kugwa kwako.

28. Pakumveka mpfuu wa oongolera ako mabwalo ako adzagwedezeka.

29. Ndi onse ogwira nkhafi, amarinyero, ndi oongolera onse a kunyanja, adzatsika ku zombo zao, nadzaima pamtunda,

30. nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira pfumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m'maphulusa,

31. nadzameta mpala, cifukwa ca iwe, nadzadzimangira ziguduli m'cuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa.

32. Ndipo pakulira adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kukulirira, ndi kuti, Wakunga Turo ndani, wakunga uyu waonongeka pakati pa nyanja?

33. Pakuturuka malonda ako m'nyanja unadzaza mitundu yambiri ya anthu, unalemeretsa mafumu a pa dziko lapansi ndi cuma cako cocuruka ndi malonda ako.

34. Muja unatyoka ndi nyanja m'madzi akuya malonda ako ndi msonkhano wako wonse adagwa pakati pako.

35. Onse okhala pa zisumbu adagwa nawe, ndi mafumu ao aopsedwa kwambiri zikhululuka nkhope zao.

36. Amalonda mwa mitundu ya anthu akunyodola, wakhala coopsetsa iwe, ndipo sudzakhalanso konse.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 27