Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 25:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako kwa ana a Amoni, nuwanenere;

3. nunene kwa ana a Amoni, Tamverani mau a Ambuye Yehova, Atero Ambuye Yehova, Popeza unati, Onyo, kunena malo anga opatulika; muja anadetsedwa ndi kunena dziko la Israyeli; muja linapasuka ndi kunena nyumba ya Yuda; muja adalowa kundende;

4. cifukwa cace taona, ndidzakupereka kwa ana a kum'mawa ukhale wao wao, kuti amange misasa yao mwa iwe, namange pokhala pao mwa iwe, iwo adzadya zipatso zako ndi kumwa mkaka wako.

5. Ndipo ndidzayesa Raba khola la ngamira, ndi ana a Amoni popumula zoweta zazing'ono; matero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

6. Pakuti atero Ambuye Yehova, Waomba manja, ndi kubvina, ndi kukondwera ndi cipeputso conse ca moyo wako, kupeputsa dziko la Israyeli,

7. cikufwa cace taona, ndakutambasulira dzanja langa, ndipo ndidzakupereka ukhale cofunkha ca amitundu, ndi kukudula mwa mitundu ya anthu, ndi kukutayikitsa m'maiko, ndidzakuononga; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 25