Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 23:28-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakupereka m'dzanja la iwo amene uwada, m'dzanja la iwo amene moyo wako ufukidwa nao;

29. ndipo adzacita nawe mwaudani, nadzalanda zonse udazigwirira nchito, nadzakusiya wamarisece ndi wausiwa; ndi umarisece wa zigololo zako udzabvulidwa, dama lako ndi zigololo zako zomwe.

30. Izi adzakucitira cifukwa watsata amitundu, ndi kucita nao cigololo, popezanso wadetsedwa ndi mafano ao.

31. Wayenda m'njira ya mkuru wako, cifukwa cace ndidzapereka cikho cace m'dzanja lako.

32. Atero Ambuye Yehova, M'cikho ca mkuru wako udzamweramo ndico cacikuru ngati mcenje; adzakuseka pwepwete, nadzakunyoza muli zambiri m'menemo.

33. Udzadzala ndi kuledzera ndi cisoni, ndi cikho codabwitsa ndi ca cipasuko, ndi cikho ca mkuru wako Samariya.

34. Udzamwa ici ndi kugugudiza, ndi kuceceta-ceceta zibade zace, ndi kung'amba maere ako; pakuti ndacinena, ati Ambuye Yehova.

35. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza wandiiwala Ine, ndi kunditaya pambuyo pako, uzisenza iwenso coipa cako ndi zigololo zako.

36. Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? uwafotokozere tsono zonyansa zao.

37. Pakuti anacita cigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anacita cigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao amuna amene anandibalira, kuti athedwe.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 23