15. Ndalozetsa nsonga ya lupanga ku zipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kucuruke; ha! analituula linyezimire, analisongoza liphe,
16. Udzisonkhanitsire pamodzi, muka ku dzanja lamanja; undandalitsa nkhondo kumuka kulamanzere; kuli konse ilozako nkhope yako.
17. Inenso ndidzaomba manja anga, ndipo ndidzakukwaniritsa ukali wanga; Ine Yehova ndanena.
18. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
19. Wobadwa ndi munthu iwe, udziikire njira ziwiri zodzera lupanga la mfumu ya ku Babulo; zonse ziwiri zicokere dziko lomwelo; nulembe cizindikilo colozera, ucilembe pa mphambano ya njira ya kumudzi.
20. Uiike njira yodzera lupanga kumka ku Raba wa ana a Amoni, ndi ya ku Yuda ku Yerusalemu, mudzi walinga.