Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 18:28-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Popeza anasamalira, natembenukira kuleka zolakwa zace zonse adazicita, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.

29. Koma nyumba ya Israyeli imanena, Njira ya Ambuye njosayenera, Inu, nyumba ya Israyeli, kodi njira zanga nzosayenera? njira zanu si ndizo zosayenera?

30. Cifukwa cace ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israyeli, yense monga mwa njira zace, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu.

31. Tayani, ndi kudzicotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israyeli?

32. Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; cifukwa cace bwererani, nimukhale ndi moyo.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 18