Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 16:60-63 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

60. Koma ndidzakumbukila Ine pangano langa ndi iwe m'masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe.

61. Pamenepo udzakumbukila njira zako ndi kucita manyazi, pakulandira abale ako akuru ndi ang'ono; ndipo ndidzakupatsa awa akhale ana ako akazi, angakhale sali a pangano lako.

62. Pakuti ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova;

63. kuti uzikumbukila ndi kucita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, cifukwa ca manyazi ako, pamene ndikufafanima zonse unazicita, ati Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 16