Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 16:59-62 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

59. Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzacita ndi iwe monga umo unacitira; popeza wapepula lumbiro ndi kutyola pangano.

60. Koma ndidzakumbukila Ine pangano langa ndi iwe m'masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe.

61. Pamenepo udzakumbukila njira zako ndi kucita manyazi, pakulandira abale ako akuru ndi ang'ono; ndipo ndidzakupatsa awa akhale ana ako akazi, angakhale sali a pangano lako.

62. Pakuti ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 16