Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 16:22-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo pa zonyansa zako zonse ndi zigololo zako sunakumbukila masiku a ubwana wako, mujaunakhala wamarisece ndi wausiwa, wobvimvinizika m'mwazi wako.

23. Ndipo kudacitika utatha zoipa zako zonse, (tsoka iwe, tsoka, ati Ambuye Yehova)

24. unadzimangira nyumba yacimphuli, unadzimangiranso ciunda m'makwalala ali onse.

25. Unamanga ciunda cako pa mphambano ziri zonse, ndipo unanyansitsa kukongola kwako, ndi kutukula mapazi ako kwa yense wopitako, ndi kucurukitsa cigololo cako.

26. Wacitanso cigololo ndi Aaigupto oyandikizana nawe, akulu thupi, ndi kucurukitsa cigololo cako kuutsa mkwiyo wanga.

27. Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kucepsa gawo lako la cakudya, ndi kukupereka ku cifuniro ca iwo akudana nawe, kwa ana akazi a Afilisti akucita manyazi ndi njira yako yoipa.

28. Unacitanso cigololo ndi Aasuri, pakuti unakhala wosakoledwa, inde unacita cigololo nao, koma sunakoledwa.

29. Unacurukitsanso cigololo cako m'dziko la Kanani, mpaka dziko la Akasidi, koma sunakoledwa naconso.

30. Ha! mtima wako ngwofoka, ati Ambuye Yehova, pakucita iwe izi zonse, ndizo nchito za mkazi wacigololo wouma m'maso.

31. Pakumanga nyumba yako yacimphuli pa mphambano ziri zonse, ndi pomanga ciunda cako m'makwalala ali onse, sunakhala ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho.

32. Ndiwe mkazi wokwatibwa wocita cigololo, wolandira alendo m'malo mwa mwamuna wace.

33. Anthu amaninkha akazi onse acigololo mphatso, koma iwe umaninkha mabwenzi ako onse mphatso zako ndi kuwalipira, kuti akudzere kucokera ku mbali zonse, kuti acite nawe cigololo.

34. M'mwemo usiyana konse ndi akazi ena m'cigololo cako; pakuti palibe wokutsata kucita nawe cigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena.

35. Cifukwa cace, wacigololo iwe, tamvera mau a Yehova:

36. Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nubvundukuka umarisece wako mwa cigololo cako ndi mabwenzi ako, ndi cifukwa ca mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawa patsa;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 16