Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 11:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane ku cipata ca kum'mawa ca nyumba ya Yehova coloza kum'mawa; ndipo taonani, pa citseko ca cipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu.

2. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m'mudzi muno;

3. ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mudzi uwu ndi mphika, ife ndife nyama.

4. Cifukwa cace uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe.

5. Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo ananti kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israyeli, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m'mtima mwanu.

6. Mwacurukitsa ophedwa anu m'mudzi muno, mwadzazanso makwalala ace ndi ophedwawo.

7. Cifukwa cace atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwace, iwo ndiwo nyama imene, ndi mudzi uwu ndiwo mphika; koma inu mudzaturutsidwa m'kati mwace.

8. Mwaopa lupanga, tsono ndidzakufikitsirani lupanga, ati Yehova Mulungu.

9. Ndipo ndidzakuturutsani m'kati mwace, ndi kukuperekani m'manja a alendo, ndi kucita maweruzo pakati panu.

10. Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani ku malire a Israyeli; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 11