Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 10:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pakuyenda akerubi anayenda ku mbali zao zinai, sanatembenuka poyenda; koma komwe udalozako mutu anatsatako, sanatembenuka poyenda.

12. Ndipo thupi lao lonse, ndi misana yao, ndi manja ao, ndi mapiko ao, ndi njinga zomwe, zinadzala ndi maso pozungulira pao, zingakhale njingazi anai aja anali nazo.

13. Kunena za njingazi, wina anazipfuulira, ndiri cimvere ine, Kunkhulirani.

14. Ndipo ali yense anali nazo nkhope zinai, nkhope yoyamba ndiyo nkhope ya kerubi, ndi nkhope yaciwiri ndiyo nkhope ya munthu, ndi yacitatu ndiyo nkhope ya mkango, ndi yacinai ndiyo nkhope ya ciombankhanga.

15. Pamenepo akerubi anakwera, ndizo zamoyo zija ndinaziona kumtsinje Kebara.

16. Ndipo pakuyenda akerubi, njinga zinayenda pambali pao, ndi pakutambasula mapiko ao akerubiwo kuuluka padziko, njingazi sizinatembenuka pambali pao.

17. Pakuima iwo zinaima izi, ndi pakukwera iwo izi zinakwera pamodzi nao; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mwa izo.

18. Ndipo ulemerero wa Yehova unacoka pa ciundo ca nyumba, nuima pamwamba pa akeruibi.

19. Ndipo akerubi anatambasula mapiko ao, nauluka padziko, ndiri cipenyere, pakucoka iwo ndi njingazi pa mbali pao; ndipo anaima pa citseko ca cipata ca kum'mawa ca nyumba ya Yehova, ndi ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unali pamwamba pao.

20. Awa ndi zamoyozo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israyeli kumtsinje Kebara, ndipo ndinadziwa kuti ndiwo akerubi.

21. Yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense mapiko anai, ndi cifaniziro ca manja a munthu pansi pa mapiko ao.

22. Ndi cifaniziro ca nkhope zao ndico nkhope zomwezo ndinaziona kumtsinje Kebara, maonekedwe ao ndi iwo eni; ali yense anayenda, nalunjika m'tsogolo.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 10