Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 8:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Wa ana a Sekaniya, mwana wa Yahazieli; ndi pamodzi naye amuna mazana atatu.

6. Ndi wa ana a Adini, Ebedi mwana wa Yonatani; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu.

7. Ndi wa ana a Elamu, Yesaya mwana wa Ataliya; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi awiri.

8. Ndi wa ana a Sefatiya, Zebadiya mwana wa Mikaeli; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi atatu.

9. Wa ana a Yoabu, Obadiya mwana wa Yehieli; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri mphambu khumi kudza asanu ndi atatu.

10. Ndi wa ana a Selomiti, mwana wa Yosifiya; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi.

11. Ndi wa ana a Bebai, Zekariya mwana wa Bebai; ndi pamodzi naye amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu.

12. Ndi wa ana a Azigadi, Yohanana mwana wa Hakatana; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu khumi limodzi.

13. Ndi a ana otsiriza a Adonikmnu, maina ao ndiwo Elifeleti, Yeueli, ndi Semaya; ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi limodzi.

Werengani mutu wathunthu Ezara 8