2. wa ana a Pinehasi, Gerisomu; wa ana a Itamara, Danieli; wa ana a Davide, Hatusi.
3. Wa ana a Sekaniya, wa ana a Parosi, Zekariya; ndi pamodzi naye, powawerenga monga mwa cibadwidwe cao, amuna zana limodzi mphambu makumi asanu.
4. Wa ana a Pahati Moabu, Elihoenai mwana wa Zerahiya; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri.
5. Wa ana a Sekaniya, mwana wa Yahazieli; ndi pamodzi naye amuna mazana atatu.
6. Ndi wa ana a Adini, Ebedi mwana wa Yonatani; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu.
7. Ndi wa ana a Elamu, Yesaya mwana wa Ataliya; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi awiri.
8. Ndi wa ana a Sefatiya, Zebadiya mwana wa Mikaeli; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi atatu.
9. Wa ana a Yoabu, Obadiya mwana wa Yehieli; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri mphambu khumi kudza asanu ndi atatu.
10. Ndi wa ana a Selomiti, mwana wa Yosifiya; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi.
11. Ndi wa ana a Bebai, Zekariya mwana wa Bebai; ndi pamodzi naye amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu.
12. Ndi wa ana a Azigadi, Yohanana mwana wa Hakatana; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu khumi limodzi.
13. Ndi a ana otsiriza a Adonikmnu, maina ao ndiwo Elifeleti, Yeueli, ndi Semaya; ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi limodzi.