Ndipo anathirirana mang'ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti cifundo cace ncosalekeza pa Israyeli. Napfuula anthu onse ndi cipfuu cacikuru, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova.