8. Ana a Zatu, mazana asanu ndi anai mphambu makumi anai kudza asanu.
9. Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.
10. Ana a Bani, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri.
11. Ana a Bebai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.
12. Ana a Asigadi, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi awiri ndi awiri.
13. Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi.
14. Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi.
15. Ana a Adini, mazana anai mphambu makumi asanu kudza anai.
16. Ana a Ateri, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi atatu.
17. Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza atatu.
18. Ana a Yora, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.
19. Ana a Hasumu, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.