Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 2:51-62 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

51. ana a Bakabuku, ana a Hakufa, ana a Haruri,

52. ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa,

53. ana a Barikosi, ana a Siseri, ana a Tama,

54. ana a Neziya, ana a Hatifa.

55. Ana a akapolo a Solomo: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,

56. ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli,

57. ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti wa Zebaimu, ana a Ami.

58. Anetini onse, ndi ana a akapolo a Solomo, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.

59. Ndipo okwera kucokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adana, Imeri, ndi awa, koma sanakhoza kuchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisrayeli:

60. ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

61. Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Kozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgileadi, nachedwa dzina lao.

62. Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa cibadwidwe cao, koma osawapeza; potero anacotsedwa ku nchito ya nsembe monga odetsedwa.

Werengani mutu wathunthu Ezara 2