3. ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.
4. Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.
5. Ana a Ara, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu.
6. Ana a Pahati Moabu, a ana a Yesuwa ndi Yoabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi awiri.
7. Ana a Elamu, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.
8. Ana a Zatu, mazana asanu ndi anai mphambu makumi anai kudza asanu.
9. Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.