16. Ana a Ateri, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi atatu.
17. Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza atatu.
18. Ana a Yora, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.
19. Ana a Hasumu, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.
20. Ana a Gibara, makumi asanu ndi anai mphambu asanu.
21. Ana a Betelehemu zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu.
22. Anthu a ku Netofa, makumi asanu mphambu asanu ndi mmodzi.
23. Anthu a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
24. Ana a Azimaveti, makumi anai mphambu awiri.
25. Ana a Kiriyati Arimu, Kefira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu.
26. Ana a Rama ndi Gaba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi.