Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 9:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo m'cinyumba ca ku Susani Ayuda anakantha, naononga amuna mazana asanu.

7. Napha Parisandata, ndi Dalifoni, ndi Asipata,

8. ndi Porata, ndi Adaliya, ndi Aridata,

9. ndi Parimasta, ndi Arisai, ndi Aridai, ndi Vaisata,

10. ana amuna khumi a Hamani mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalanda zofunkha.

11. Tsiku lomwelo anabwera naco kwa mfumu ciwerengo ca iwo ophedwa m'cinyumba ca ku Susani.

12. Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkuru Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m'cinyumba ca ku Susani, ndi ana amuna khumi a Hamani; nanga m'maiko ena a mfumu munacitikanji? pempho lanu ndi ciani tsono? lidzacitikira inu; kapena mufunanjinso? kudzacitika.

13. Nati Estere, Cikakomera mfumu, alole Ayuda okhala m'Susani acite ndi mawa lomwe monga mwa lamulo la lero; ndi ana amuna khumi a Hamani apacikidwe pamtengo.

14. Ndipo mfumu inati azicita motero, nalamulira m'Susani, napacikidwa ana amuna khumi a Hamani.

Werengani mutu wathunthu Estere 9